Mukhonza kugwiritsa ntchito Facebook ndi zipangizo zina za makono kuti muthandize magulu kapena anthu othandizira kuthesa nkhanza kwa amayi ndi ana za nkhanza zomwe mukuziwona (kuphatikiza ngati muli a komiti) kapena zikukuchitikirani, maka kuchokera kwa achibale kapena anansi, ngakhale mabwana, aziphunzitsi ndi ena otero.
Mukhonzanso kudziwitsa magulu kapena anthu othandiza kupititsa ana ku sukulu za ana omwe (mu)akulephera kupita ku sukulu chifukwa chosowa chithandizo kapena nkhanza koma (mu)akufunako.
Chonde, kumbukirani kuti kulembetsa uku ndi kwa chinsisi ndi cholinga kuti musapwetekeke.

1. Ndimaona/ndimachitiridwa nkhanza
Lembetsani nkhani zokhuza nkhanza, kuzembetsa anthu, kukwatira ana, kugwiririra ana, kugwiritsa ana ntchito zoposa nsinkhu ndi zina zotero, maka zochitikira kwa amene akulephera kuwulura.

2. Pali/ndine mwana amene (ndi)akulephera kupita ku sukulu
Lembetsani nkhani zokhuza ana okhawo amene (mu)akulephera kupita ku sukulu koma (mu)akufunako apa. Dziwani kuti ana amene (mu)alibe chidwi ndi sukulu saali oyenera kulembetsedwa.

3. Onani Zotsatira
Zawoneni zotsatira pakatha masiku awiri chilembetsereni.
Ngati nkhani yanu ili yayikulu kwambiri, agent akhonza kukutsatirani pasanathe masiku awiri kuti akuwuzeni zotsatira.
Pokumva zotsatira, muzawuzidwa zoyenera kuchita.