Chonde, kumbukirani kuti simukuyenera kulembetsa dzina lanu komanso nambara ya foni. Ngati muli kale ndi nambara ya Visitor, itchuleni, kenako pitani pa funso 2, kenako ndikumapitiliza.

1. Nambara yanu ngati Visitor
Choyambirira, awuzeni a agent akuwerengereni nambara yanu ngati Visitor ndipo akupatseni ka pepara kolembadwa nambarayo.
2. Ndinu mwini nkhani kapena wina?
~ Ndine
~ Wina
3. Fotokozani mbiri ya mwanayo
Fotokozani zokhuza zinthu izi;
Mudzi umene amachokera
Ngati ali wamwamuna kapena wa mkazi
Zaka zake zakubadwa
Kalasi yomwe ali kapena anali
Mbiri yake pa nkhani za maphunziro, maka kulimbikira kwake mungakufotokoze motani?
Chonde, mubwerenso pakatha ma hora 24 (tsiku limodzi) kapena musiye njira yomwe agent angathe kulumikizana nanu