Kwa amene muli ndi chidwi ndi maphunziro kapena Kuphunzira ndi kupeza ntchito za manja ndi zina zotero!
Tsopano mukhonza kupeza maphunziro owonjezera kuyambira ku sukulu ya mkomba phala (nazare), primary, secondary mpaka ya kwacha ndi cholinga chofuna kuzama zomwe zaphunziridwa ku sukulu kapena kupeza upangiri okuthandizani kupeza ntchito.
Kupatula maphunziro, mukhonza kufufuza ndi kufunsira ntchito.
Jambulitsani Kanema Okhuza Maphunziro ndi Ntchito Pano

1. Maphunziro a mkomba phala (Kindergarten & Early Childhood Development)
Mukhonza kuwalembetsera ana anu ndi kuwabweretsa kuzaphunzira maphunziro owonjezera a ku sukulu ya mkomba phala.
Ana akhonza kupeza maphunziro monga chizungu, masamu ndi zina zotero.

2. Maphunziro a ku primary school
Mukhonza kulembetsa apa kuti mwana wanu kapena nokha mupeze maphunziro owonjezera aku primary.

3. Maphunziro aku secondary school
Mukhonza kulembetsa apa kuti mupeze maphunziro owonjezera aku secondary school

4. Maphunziro a za manja ndi zina (Tertiary Education, Technical, Vocational and Labour Skills)
Lembetsani apa kuti mupeze maphunziro owonjezera aku college kapena ntchito za manja ndi zina za upangiri osiyanasiyana monga kuphika, kumanga nyumba, kuwotcherela, kupenta, ulonda, kuyendetsa galimoto ndi zina zotero.

5. Maphunziro a kwacha (Civic Education)
Mukhonza kulembetsa apa kuti mupeze maphunziro owonjezera aku sukulu ya kwacha (Civic adult education) monga kulemba ndi kuwerenga ndi zina zotero.

6. Kufufuza ndi kufunsira ntchito (job searching and vacancies)
Mukhonza kufufuza ndi kufunsira ntchito zosiyanasiyana za ku mtima kwanu pa masamba osiyanasiyana m’Malawi muno.
Mukhonzanso kulembetsa ntchito zomwe mukufuna ndi mbiri ya upangiri wanu (CV) kuti mukhale pa mndanda wa osaka ntchito omwe udzayikidwe pa Facebook, LinkedIn, Twitter ndi masamba ena omwe mabwana amapezeka, ndipo atha kuwona. Chonde dziwani kuti m’ndanda uwu ndi wa m’chigulu, komanso ndi kutsatsa chabe.