Jambulitsani Kanema Okhuza Maphunziro ndi Ntchito

Chonde, kumbukirani kuti simukuyenera kulembetsa dzina lanu komanso nambara ya foni. Ngati muli kale ndi nambara ya Visitor, itchuleni, kenako pitani pa funso 2, kenako ndikumapitiliza.


1. Nambara yanu ngati Visitor

Choyambirira, awuzeni a agent akuwerengereni nambara yanu ngati Visitor ndipo akupatseni ka pepara kolembadwa nambarayo.

2. Ndinu mwini nkhani kapena wina?

~ Ndine
~ Wina

3. Mtundu wa nkhani

3.1. Kuwunikira mzeru anthu ena

Mukhonza kujambulitsa kanema ofotokoza masomphenya, mfundo/msanamira, ngakhale njira zomwe munatsata kuti muthane ndi zopinga kapena mufike patali ndi ntchito yanu kuti ena atseguke m’maso kapena aphunzire nawo.

Mumagwira kapena munayesera kugwira ntchito yanji?

Ndinu okhutitsidwa motani ndi ntchito yanuyo (zimayenda/zinayenda bwino? Mumasangalala/munasangalala? Motani)

Kodi pa chiyambi, masomphenya anu, kapena chiyembekezo chanu chinali chotani? Mumafuna kapena mumaganiza kuti mupindula motani?

Ndiye zimenezi zinatheka? Munapindula motani ndipo zakubweretserani zotsatira zotani?

Kodi kweni kweni chinapangitsa ndi chani kuti zikhale choncho? – Ndi njira ziti zomwe munatsata kapena mwayi uti umene unapangisa kuti izi zitheke (chonde, tchulani zochitika osati zachikhulupiliro malingana chipembezo kapena chikhalidwe)

3.2. Kupempha mzeru anthu ena

Mukhonza kujambulitsa kanema kuti ena amvetsetse pomwe panasokonekera/pamasokonekera kuti mukwaniritse kapena mufike pomwe mumafuna, kuti mwina ena atadziwa akhonza kukuthandizani mzeru kapena mu njira ina.

Mumagwira kapena munayesera kugwira ntchito yanji?


Ndinu okhutitsidwa motani ndi ntchito yanu?

Kapena kuti ndi chani chomwe mumawona kuti mumatha kwambiri, zinthu zomwe mumapanga kapena munapanga, zochititsa kaso, za luntha, za ukadawulo kapena zopeleka chilimbikiso?


Kodi pa chiyambi, masomphenya anu, kapena chiyembekezo chanu chinali chotani? Mumafuna kapena mumaganiza kuti mupindula motani?

Ndiye zimenezi zinatheka? Pano zili pati? Ngati sizinatheke, chinachitika/chikumachitika ndi chani kweni kweni?

Nanga kulephereka kwa zinthu kwakubweretserani kapena kunabweretsa zotsatira zotani, kukhuzana ndi moyo wanu kapena banja lanu?

Kodi kweni kweni chinapangitsa/chimapangitsa ndi chani kuti zikhale choncho? Kapena kuti ndi chani chimene chinasowekera kapena chimasowekera kuti musathe kupita patsogolo ndi ntchitoyo?

Mwachitapo chani kuti muthane ndi vutoli?

Nanga mukuganiza kuti panafunika kuchitapo chani kuti vutoli lithe? Mukufuna thandizo lotani?

Ngati simunayankhulane ndi nkozi wa njirayi, mubwerenso pakatha ma hora 24 (tsiku limodzi) kapena musiye njira yomwe agent angathe kulumikizana nanu kuti akudziwitseni zotsalira kapena zomwe zadumphidwa.

Design a site like this with WordPress.com
Get started