ZOPEZEKA PA INTERNET

Takulandirani! Lowani pa masamba ndi zipangizo zopezeka pa internet zomwe zikugwirizana ndi zomwe mukufuna kufufuza kapena kuchita kalondolondo m’musimu.

Dziwani kuti ntchito yayikulu ya tsamba lino la COMP@SS ndi kusonkhanitsa masamba ndi zipangizo za makono (websites and apps) zopezeka pa internet zomwe anthu okhala m’midzi akhonza kugwiritsa ntchito, ndi kuthandizira akonzi ake kuchita kalondolondo wa amene agwiritsa nawo ntchito komanso m’mene athandizikira. Akonziwa azidzalipira kuti apeze ma ripoti amenewa kuyambira m’chaka cha 2025 ntchito yowumba tsambali ikazatha, ngati gawo limodzi la bizinesi za 3rdWorld zothandizira ntchito za kafukufuku ndi kufewetsa kachitidwe ka zinthu. Dziwani kuti palibe ubale wina uliwonse ndi akonzi a masamba ndi zipangizo zimenezi, ndipo palibe dongosolo la zolandiritsa zinthu m’malingana ndi zomwe mwafufuza.

ZAULIMI

Ulimi nthawi zina ndi ovuta, okhumudwitsa, onerani m’mene ena akuthanirana nazo. Fufuzani mitengo ya mbewu/ziweto. Gwiritsani ntchito njira za makono kuti mudziwe matenda a mbewu/ziweto ndi kuphweketsa zochitika zina pa ulimi.

ZA LUSO LOKOPA ALENDO NDI ZOSAMALIRA CHILENGEDWE

Kodi muli ndi luso la za chikhalidwe monga kuyimba, kuvina, kujambula; muli ndi luntha kapena mumachita ntchito zokopa alendo ndi zosamalira za chilengedwe kudera kwanu? Apa ndi pomwe mukhonza kuzamitsira luso kapena luntha lanu, kulengezetsa malonda kapena kufalitsa uthenga komanso kuthandizira ntchito za kalondolondo wa chilengedwe chopezekera m’dera lanu.

ZA NKHANZA KWA A MAYI NDI ANA OSOWA POGWIRA

…pomwe mukhonza kulembetsa ndi kulengezetsa nkhanza kwa a mayi ndi ana osowa pogwira zomwe mumaziwona kapena kukuchitikirani, kuphatikiza ana amene akulephera kupita ku sukulu chifukwa chosowa chithandizo.

ZA MAPHUNZIRO NDI KUSAKA NTCHITO

…pomwe mukhonza kupeza maphunziro kuyambira ku sukulu ya mkomba phala (nazare), mpaka ya kwacha komanso mukhonza kufufuza ntchito

ZA MATENDA, UMOYO NDI UKHONDO

…pomwe mukhonza kupeza kapena kupeleka uphungu wa za umoyo ndi mankhwala a chilengedwe komanso za ukhondo. Mukhonzanso kuthandizira ntchito za kalondolondo wa za umoyo m’dera lanu.

ZA MPHAMVU ZA MAGETSI NDI NJIRA ZOPHIKIRA

…pomwe mukhonza kufufuza za mphamvu za magetsi ndi njira zophikira za makono.

Design a site like this with WordPress.com
Get started