Chonde, kumbukirani kuti simukuyenera kulembetsa dzina lanu komanso nambara ya foni. Ngati muli kale ndi nambara ya Visitor, itchuleni, kenako pitani pa funso 2, kenako ndikumapitiliza.

1. Nambara yanu ngati Visitor
Choyambirira, awuzeni a agent akuwerengereni nambara yanu ngati Visitor ndipo akupatseni ka pepara kolembadwa nambarayo.
2. Ndinu mwini nkhani kapena wina?
~ Ndine
~ Wina
3. Mtundu wa nkhani
3.1. Kuwunikira mzeru anthu ena
Mukhonza kujambulitsa kanema ofotokoza masomphenya, mfundo/msanamira, ngakhale njira zomwe munatsata kuti muthane ndi zopinga kapena mufike patali ndi ntchito yanu kuti ena atseguke m’maso kapena aphunzire nawo.
Mumalima/munalima mbewu/ziweto zanji?
Ndinu okhutitsidwa motani ndi ulimi wanuwo (zimayenda/zinayenda bwino? Mumasangalala/munasangalala? Motani)
Kodi pa chiyambi, masomphenya anu, kapena chiyembekezo chanu chinali chotani? Mumafuna kapena mumaganiza kuti mupindula motani?
Ndiye zimenezi zinatheka? Munapindula motani ndipo zakubweretserani zotsatira zotani?
Kodi kweni kweni chinapangitsa ndi chani kuti zikhale choncho? – Ndi njira ziti zomwe munatsata kapena mwayi uti umene unapangisa kuti izi zitheke (chonde, tchulani zochitika osati zachikhulupiliro malingana chipembezo kapena chikhalidwe)
3.2. Kupempha mzeru anthu ena
Mukhonza kujambulitsa kanema kuti ena amvetsetse pomwe panasokonekera/pamasokonekera kuti mukwaniritse kapena mufike pomwe mumafuna, kuti mwina ena atadziwa akhonza kukuthandizani mzeru kapena mu njira ina.
Mumalima/munalima mbewu/ziweto zanji?
Ndinu okhutitsidwa motani ndi ulimi wanu?
Kodi pa chiyambi, masomphenya anu, kapena chiyembekezo chanu chinali chotani? Mumafuna kapena mumaganiza kuti mupindula motani?
Ndiye zimenezi zinatheka? Ngati sizinatheke, chinachitika/chikumachitika ndi chani kweni kweni?
Munapindula kapena kuluza motani ndipo zakubweretserani zotsatira zotani?
Kodi kweni kweni chinapangitsa ndi chani kuti zikhale choncho?
Mwachitapo chani kuti muthane ndi vutoli?
Ngati simunayankhulane ndi nkozi wa njirayi, mubwerenso pakatha ma hora 24 (tsiku limodzi) kapena musiye njira yomwe agent angathe kulumikizana nanu kuti akudziwitseni zotsalira kapena zomwe zadumphidwa.