
Ndi chani?
Njira yomwe ikupezeka ngati tsamba la pa makina a internet komanso malo ochitira malonda m’midzi yomwe anthu okhala m’madera akumidzi mukhonza kugwiritsira ntchito makina a internet ndi zipangizo zina za makono pofuna kupeza mayankho a zopinga ndi kuphweketsa kachitidwe ka ntchito zanu maka za malonda, ulimi, maphunziro; kufalisira uthenga komanso kuchita kalondolondo othandizira ntchito za kafukufuku wa zochitika za pa khomo ngakhale m’mudzi mwanu, kudzera kwa agent.
Iyi ndi njira yomwe ikukonzedwa komanso kuyesedwa ndi 3rdWorld Xplorations ngati njira yake imodzi yothandizira ntchito zakafukufuku kudzera mu timabizinesi ting’onoting’ono tofuna kufewesa kachitidwe ka zinthu kwa anthu okhala m’madera akumidzi kudzera kwa anthu amene akufuna kukhala ma agent ake.
Ntchito yake
Village Internet ndi njira imodzi ya njira zingapo za 3rdWorld Xplorations zothandizira ntchito za kafukufuku maka za chitukuko cha m’madera akumidzi ndi za chilengedwe.
Kumbali ya anthu okhala m’madera a ku midzi, Village Internet ndi njira yomwe 3rdWorld Xplorations ikufuna kugwiritsa ntchito popanga nanu malonda osiyanasiyana, maka a zaulimi.
Kagwiridwe ntchito kake
Anthu okhala m’madera a kumidzi akhonza kugula ndi kugulitsa malonda pa mtengo wa m’tawuni potenga nawo gawo mu kalondolondo (kalembera) othandizira ntchito za kafukufuku yemwe mabungwe ndi boma akhonza kugwiritsa ntchito kuti adziwe gwero la mavuto a chitukuko m’mudzi mwanu ndi kupeza njira zoyenera.
Village Internet ili ndi magawo angapo omwe ali m’magawo osiyanasiyana a chitukuko monga m’musimu

OmniScope Stories&Stats
Bwalo la pa intaneti lo ululira ndi kuchitira kalondolondo wa nkhanza kwa amayi ndi ana osowa pogwira, komanso kalondolondo wa zithandizo ndi ntchito zofuna kuthesa nkhanzazo

Umodzi Farms
Bwalo la pa intaneti ndi mabwalo a m’midzi omwe alimi akhonza kupezelapo uthenga kapena ulangizi ndi kuchita kalondolondo wa ulimi wawo pofuna kuzama mu kalimidwe komanso kulondoloza ndi kuyika malonda a zokolora pa msika wa pa intaneti

Chikhalidwe eco-centers
Bwalo la pa intaneti ndi mabwalo a m’midzi ochitira kalondolondo, kafukufuku ndi kupititsira patsogolo ntchito ndi zaluso zosamala chilengedwe ndi kusunga chikhalidwe/mzeru za makolo komanso malonda ake ndi ntchito zake zokopa alendo, zoyambisidwa ndi anthu a m’midzi