Tsopano anthu onenedwa kuti akupenga kapena akutaya nthawi ndi zaluso zogwiritsa ntchito zinyalala, za chikhalidwe komanso khama losamilira/kuteteza chilengedwe akhonza kupeza anansi!
Mukhonza kutsatsa malonda a zaluso lanu la za chikhalidwe, zokopa alendo ndi zosamalira chilengedwe kugwiritsa ntchito Facebook ndi zipangizo zina za makono.
Mukhonzanso kuchita ndi kufalisira kalondolondo wa za ntchito zanu zosamalira chilengedwe ndi zokopa alendo kuti muthandize magulu kapena anthu othandizira ntchito zanu kupeza njira zabwino zokuthandizirani.

1. Ndili ndi luso la za chikhalidwe
Mukhonza kulembetsa apa ngati muli ndi luso la za chikhalidwe monga kuyimba, kuvina, kusema, kuphika zakudya za makolo ndi zina zotero.

2. Ndili ndi luso logwiritsa ntchito zinyalala kapena za chilengedwe
Mukhonza kulembetsa apa ngati muli ndi luso logwiritsa ntchito zinyalala monga ma plastic, mabotolo, zitsulo, zakudya zotsala, ndowe, zomera, mpweya, mphamvu ya dzuwa, mphepo, madzi ndi zina zotero.

3. Ndimagwira ntchito zosamalira/kuteteza za chilengedwe mozipeleka
Mukhonza kulembetsa apa ngati mumagwira ntchito mozipeleka, yothandizira kusamala chilengedwe monga nkhalango, nyanja, nyama za nkhalango kuphatikiza nsomba ndi mbalame ndi zina zotero.

3. Ndimagwira ntchito/bizinesi ya zokopa alendo
Mukhonza kulembetsa apa ngati mumagwira ntchito kapena kupanga bizinesi ya zokopa alendo.