Kulembetsa

Chonde, kumbukirani kuti simukuyenera kulembetsa dzina lanu komanso nambara ya foni. Ngati muli kale ndi nambara ya Visitor, itchuleni, kenako pitani pa funso no. 3, ndikumapitiliza.


Mvetserani mafunso onse pa kanema oyamba ali m’musimuyu. Kenako, pafunso lililonse, mverani mpaka kumapeto a funso lonse (kanema yense) musanayambe kuyankha.

Mukhonza kugwiritsa ntchito kanema kuti muyankhe mafunso ofunsidwa polembetsa

1. Nambara yanu ngati Visitor

Choyambirira, awuzeni a agent akuwerengereni nambara yanu ngati Visitor ndipo akupatseni ka pepara kolembadwa nambarayo.

2. Dzina la mudzi ndi mbali yake

Tchulani dzina la mudzi wanu, nyakwawa ndi gurupu, komanso mbali ya mudzi yeni yeni yomwe mumapezekera

2.1. Kuphatikiza, tchulani ngati ndinu okhazikika m’mudzimo, ongobwera kapena ndinu mulendo

3. Zaka zakubadwa

Tchulani zaka zanu zakubadwa kapena chaka chomwe munabadwa

4. Pomwe munalekezera maphunziro

Tchulani kalasi yomwe munalekezera ku mbali ya maphunziro

5. Njira zopezera ndalama

5.1. Tchulani njira zopezera ndalama zomwe mwagwiritsa ntchito m’miyezi 12 yapitayi kuchoka mwezi uno.

Yambani ndi ntchito zomwe mumagwira nthawi zonse kapena zambiri kumaliza zopanga pa kanthawi. Ngati uli ulimi, tchulani mbewu zake.

Ngati palibe koma mumalima mbewu zokudya pa khomo panu ngati kholo, tchulani ulimi omwe mwachita mu miyize 12 yapitayi.

Ngati palibiletu chomwe mwakhala mukuchita mu miyize 12 yapitayi, tchulani kuti “palibe” ndipo pitani pa funso 5.3.

Ngati muli pa sukulu, tchulani kalasi ndi dzina la sukulu yomwe muli.

5.2. Tchulani njira zopezera ndalama zomwe mwagwiritsa ntchito m’masiku 30 athawa kuchokera lero.

Yambani ndi ntchito zomwe mumagwira nthawi zonse kapena zambiri kumaliza zopanga pa kanthawi. Ngati uli ulimi, tchulani mbewu zake.

5.3. Tchulani njira zopezera ndalama zomwe mwakhala mukukhumbira kugwiritsa ntchito koma mwakhala mukulephera.

Ntchito izi ndi kuphatikiza zomwe mukukhumbira mutayamba pakadali pano kapena mtsogolo.

Ngati uli ulimi, tchulani mbewu zake.

6. Tchulani njira zopezera ndalama zomwe mwagwiritsa ntchito m’masiku 7 athawa kuchokera lero.

7. Zikomo polembetsa, sankhani kupitiliza m’musimu! 😊

Design a site like this with WordPress.com
Get started